Genesis 32:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono adauzanso mnyamata wake wachiŵiri mau omwewo, ndi wachitatu, mpaka onse amene ankayenda motsogoza zoŵeta. Adaŵauza kuti, “Zimenezi ndizo mukauze Esau, mukakumana naye.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anauzanso wachiwiri ndi wachitatu, ndi onse anatsata magulu, kuti, Muzinena kwa Esau chotero, pamene mukomana naye:
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anawuza mawu omwewo kwa wachiwiri, wachitatu ndi ena onse amene ankayenda motsogoza ziwetozo kuti, “Inunso munene zomwezo kwa Esau mukakumana naye.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anauzanso waciwiri ndi wacitatu, ndi onse anatsata magulu, kuti, Muzinena kwa Esau cotero, pamene mukomana naye: