Genesis 32:22 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Usiku womwewo Yakobe adadzuka natenga akazi ake aŵiri, ndi adzakazi ake aŵiri aja, pamodzi ndi ana ake khumi ndi mmodzi, naoloka mtsinje wa Yaboki padooko pake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anauka usiku womwewo, natenga akazi ake awiri, ndi adzakazi ake awiri, ndi ana ake amuna khumi ndi mmodzi, naoloka pa dooko la Yaboki.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Usiku umenewo Yakobo anauka natenga akazi ake awiri, antchito ake awiri ndi ana ake aamuna khumi ndi mmodzi nawoloka pa dooko la mtsinje wa Yaboki.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anauka usiku womwewo, natenga akazi ace awiri, ndi adzakazi ace awiri, ndi ana ace amuna khumi ndi mmodzi, naoloka pa doko la Yaboki.