Genesis 32:28 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Munthu uja adati, “Dzina lako silidzakhalanso Yakobe. Walimbana ndi Mulungu ndi anthu, ndipo wapambana. Motero dzina lako lidzakhala Israele.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anati, Dzina lako silidzatchedwanso Yakobo, koma Israele, chifukwa unayesana naye Mulungu ndithu, ndipo unapambana.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamenepo munthuyo anati, “Dzina lako silidzakhalanso Yakobo koma Israeli, chifukwa walimbana ndi Mulungu ndi anthu ndipo wapambana.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anati, Dzina lako silidzachedwanso Yakobo, koma Israyeli, cifukwa unayesana naye Mulungu ndithu, ndipo unapambana.