Genesis 32:29 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pomwepo Yakobe adati, “Choncho nanunso tandiwuzani dzina lanu.” Koma munthuyo adati, “Chifukwa chiyani ukundifunsa dzina?” Ndipo pompo munthu uja adadalitsa Yakobe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Yakobo ndipo anafunsa iye, nati, Undiuze ine dzina lako. Ndipo iye anati, Undifunsa dzina chifukwa ninji? Ndipo anamdalitsa iye pamenepo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yakobo anati, “Chonde, uzeni dzina lanu.” Koma munthuyo anati, “Chifukwa chiyani ukundifunsa dzina?” Kenaka anamudalitsa pomwepo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Yakobo ndipo anafunsa iye, nati, Undiuze ine dzina lako. Ndipo iye anati, Undifunsa dzina cifukwa ninji? Ndipo anamdalitsa iye pamenepo.