Genesis 32:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adaŵalangiza kuti akauze Esau kuti, “Ine Yakobe mtumiki wanu ndinkakhala kwa Labani, ndipo ndakhalitsako mpaka tsopano lino.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anauza iwo kuti, Mukanene chotere kwa mbuyanga Esau: Atero Yakobo kapolo wako, ndakhala pamodzi naye Labani, ndipo ndakhalabe kufikira tsopano lino:
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anawalangiza kuti, “Zimene mukanene ndi izi kwa mbuye wanga Esau: ‘Mtumiki wanu Yakobo akuti, Ine ndakhala ndi kukhala ndi Labani mpaka tsopano.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anauza iwo kuti, Mukanene cotere kwa mbuyanga Esau: Atero Yakobo kapolo wako, ndakhala pamodzi naye Labani, ndipo ndakhalabe kufikira tsopano line: