Genesis 32:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo Yakobe adachita mantha kwambiri ndi kutaya mtima. Motero anthu amene anali nawo adaŵagaŵa m'magulu aŵiri, pamodzi ndi nkhosa, mbuzi, ng'ombe ndiponso ngamira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yakobo anaopa kwambiri, navutidwa; ndipo anagawa anthu anali nao ndi nkhosa ndi zoweta, ndi ngamira, zikhale makamu awiri;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yakobo anali ndi mantha ndi nkhawa yayikulu kwambiri. Tsono anagawa anthu onse amene anali naye, ndiponso nkhosa, mbuzi, ngʼombe ndi ngamira mʼmagulu awiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yakobo anaopa kwambiri, nabvutidwa; ndipo anagawa anthu anali nao ndi nkhosa ndi zoweta, ndi ngamila, zikhale makamu awiri;