Genesis 32:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo Yakobe adayamba kupemphera. Adati, “Mulungu wa kholo langa Abrahamu, Mulungu wa bambo wanga Isaki, mundimve ine! Inu Chauta mudandiwuza kuti, ‘Bwerera ku dziko lako, dziko la abale ako, ndidzasamala kuti zinthu zikuyendere bwino.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yakobo anati, Mulungu wa atate wanga Abrahamu, Mulungu wa atate wanga Isaki, Yehova, amene munati kwa ine, Bwera ku dziko lako, ndi kwa abale ako, ndipo ndidzakuchitira iwe bwino:
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamenepo Yakobo anapemphera, “Haa, Mulungu wa kholo langa Abrahamu, Mulungu wa abambo anga Isake, Aa Yehova amene munati kwa ine, ‘Bwerera ku dziko la kwanu ndi kwa abale ako, ndipo ndidzakuchitira zabwino.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yakobo anati, Mulungu wa atate wanga Abrahamu, Mulungu wa atate wanga Isake, Yehova, amene munati kwa ine, Bwera ku dziko lako, ndi kwa abale ako, ndipo ndidzakucitira iwe bwino: