Genesis 33:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yakobe adati, “Ai chonde, ngati mwandikomera mtima, landirani mphatso yanga. Ine ndikamaona nkhope yanu, ndiye ngati ndaona nkhope ya Mulungu, poti mwandilandira chonchi ndi manja aŵiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yakobo anati, Iaitu, ngatitu ndapeza ufulu pamaso panu, mulandire mphatso yanga pa dzanja langa; pakuti popeza ndinaona nkhope yanu, monga anthu aona nkhope ya Mulungu, ndipo inu mwandivomereza ine.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yakobo anati, “Chonde musatero. Ngati mwandikomera mtima, landirani mphatso yangayi kuchokera kwa ine. Pakuti ndi mmene mwandirandira bwinomu, ine ndikamaona nkhope yanu ndikuchita ngati ndikuona nkhope ya Mulungu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo! Yakobo anati, Iaitu, ngatitu ndapeza ufulu pamaso panu, mulandire mphatso yanga pa dzanja langa; pakuti popeza ndinaona nkhope yanu, monga anthu aona nkhope ya Mulungu, ndipo inu mwanelibvomereza ine.