Genesis 33:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chonde landirani mphatso ndakutengeraniyi. Mulungu adandikomera mtima, ndipo adandipatsa zosoŵa zanga zonse.” Adapitirira kumuumiriza, mpaka Esau adalandira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Landiranitu mdalitso wanga umene wafika kwa inu, pakuti Mulungu wandichitira ine zaufulu, ndipo zanganso zindifikira. Ndipo anamkakamiza, nalandira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chonde, landirani mphatso imene ndakutengeraniyi, popeza Mulungu wandikomera mtima kwambiri moti ndili ndi zonse zimene ndizifuna.” Ndipo popeza kuti Yakobo anamuwumiriza, Esau analandira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Landiranitu mdalitso wanga umene wafika kwa inu, pakuti Mulungu wandicitira ine zaufulu, ndipo zanganso zindifikira. Ndipo anamkakamiza, nalandira.