Genesis 33:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Yakobe adati, “Mbuyanga, mukudziŵa kuti anaŵa atopa, ndipo ndiyenera kusamalanso nkhosa ndi ng'ombe zimene zili ndi tiana. Ndikazikusa mofulumira kwambiri, ngakhale tsiku limodzi lokha, zifa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anati kwa iye, Mbuyanga adziwa kuti ana ali ambowa, ndipo nkhosa ndi zoweta ndili nazo zilinkuyamwitsa: ndipo akathamangitsa tsiku limodzi zoweta zonse zidzafa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Yakobo anati kwa iye, “Mbuye wanga, inu mudziwa kuti anawa ndi a nthete ndiponso ndiyenera kusamalira nkhosa ndi ngʼombe zimene zikuyamwitsa ana awo. Ngati ndizimenya kuti zifulumire, tsiku limodzi lokha nyamazo zidzafa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anati kwa iye, Mbuyanga adziwa kuti ana ali ambowa, ndipo nkhosa ndi zoweta ndiri nazo zirinkuyamwitsa: ndipo akathamangitsa tsiku limodzi zoweta zonse zidzafa.