Genesis 33:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo Esau adati, “Tsono undilole kuti ndikusiyire anthu anga enaŵa.” Koma Yakobe adati, “Iyai mbuyanga, zimenezo sizifunika kwenikweni, ndingofuna kukukondwetsani.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Esau anati, Ndikusiyire anthu ena amene ali ndi ine. Ndipo iye anati, Chifukwa chanji? Ndipeze ine ufulu pamaso pa mbuyanga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Esau anati, “Ndiye bwanji ndikusiyireko ena mwa anthu anga.” Koma Yakobo anati, “Koma muchitiranji zimenezi? Chachikulu nʼkuti mwandilandira bwino, mbuye wanga.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Esau anati, Ndikusiyire anthu ena amene ali ndi ine, Ndipo iye anati, Cifukwa canji? ndipeze ine ufulu pamaso pa mbuyanga.