Genesis 33:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake Yakobe adakafika bwino ku mzinda wa Sekemu m'dziko la Kanani, atabwerera kuchokera ku Mesopotamiya. Adamanga mahema pamalo pena, poyang'anana ndi mzindawo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yakobo anafika ndi mtendere kumudzi wa Sekemu umene uli m'dziko la Kanani, pamene anachokera ku Padanaramu; namanga tsasa pandunji pa mudzipo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mmene ankabwerera kuchokera ku Padanaramu, Yakobo anafika ku Salemu, mzinda wa Sekemu ku Kanaani. Anamanga msasa pamalopo moyangʼanana ndi mzindawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yakobo anafika ndi mtendere ku mudzi wa Sekemu umene uli m'dziko la Kanani, pamene anacokera ku Padanaramu; namanga tsasa pandunji pa mudzipo.