Genesis 33:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Esau atayang'ana, adaona akazi ndi ana omwe aja, ndipo adamufunsa kuti, “Anthu aŵa ali ndi iweŵa nga yani?” Yakobe adayankha kuti, “Aŵa, mbuyanga, ndi ana amene Mulungu adandipatsa mwa chifundo chake.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anatukula maso ake nawaona akazi ndi ana; nati, Ndani awa ali ndi iwe? Ndipo iye anati, Ndiwo ana amene Mulungu anakomera mtima kumpatsa kapolo wanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka Esau ataona amayi ndi ana awo anamufunsa Yakobo kuti, “Kodi anthu amene uli nawowa ndi a ndani?” Yakobo anayankha kuti, “Awa ndi ana amene Mulungu, mwa kukoma mtima kwake, wapereka kwa mtumiki wanune.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anatukula maso ace nawaona akazi ndi ana; nati, Ndani awa ali ndi iwe? Ndipo iye anati, Ndiwo ana amene Mulungu anakomera mtima kumpatsa kapolo wanu.