Genesis 34:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo mnyamatayo adafulumira kuchita zimene zinkafunikazo, chifukwa choti adaamkonda kwambiri mwana wa Yakobeyo. Sekemu anali wotchuka kwambiri m'banja lakwaolo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mnyamatayo sanachedwe kuchichita popeza anakondwera ndi mwana wake wamkazi wa Yakobo; ndipo iye anali wolemekezedwa woposa onse a pa banga la atate wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mnyamata uja amene anali wolemekezeka kwambiri pa banja lake lonse, sanachedwe kuchita mdulidwe popeza anamukonda kwambiri mwana wa Yakobo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mnyamatayo sanacedwa kucicita popeza anakondwera ndi mwana wace wamkazi wa Yakobo; ndipo iye anali wolemekezedwa woposa onse a pa banja la atate wace.