Genesis 34:21 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Anthu aŵa ndi abwenzi athu. Motero tiŵalole kuti akhale m'dziko mwathu muno, kuti azichita malonda mwaufulu. Dzikoli ndi lalikulu ndipo lingathenso kuŵakwanira iwowo. Tiyeni tizikwatirana nawo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Anthu amenewa ali amtendere pamodzi ndi ife; chifukwa chake akhale m'dzikomo, achite malonda m'menemo: pakuti taonani dzikolo lili lalikulu lokwanira iwo; tidzitengere ana ao akazi akhale akazi athu, tiwapatse amenewa ana athu akazi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo anati, “Anthu awa ndi a mtendere. Aloleni kuti akhale mʼdziko mwathu muno nachitamo malonda. Dzikoli lili ndi malo ambiri woti iwo nʼkukhalamo. Tingathe kukwatira ana awo aakazi ndipo angathe kukwatira ana athu aakazi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Anthu amenewa ali amtendere pamodzi ndi ife; cifukwa cace akhale m'dzikomo, acite malonda m'menemo: pakuti taonani dzikololirilalikurulokwaniraiwo; tidzitengere ana ao akazi akhale akazi athu, tiwapatse amenewa ana athu akazi.