Genesis 34:27 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ana ena a Yakobe adafika pa ophedwa aja nafunkha zonse zamumzindamo, chifukwa choti anali atamgwiririra mlongo wao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ana amuna a Yakobo anadza kwa ophedwa nafunkha mudzi chifukwa anamuipitsa mlongo wao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ana a Yakobo anafika kwa anthu ophedwawo ndi kututa katundu mu mzindawo chifukwa anagwiririra mlongo wawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ana amuna a Yakobo anadzakwa ophedwa nafunkhamudzi cifukwa anamuipitsa mlongo wao.