Genesis 34:30 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yakobe adauza Simeoni ndi Levi kuti, “Hi, mwandiputira nkhondo. Dzina langa laipa pakati pa anthu a dziko lino, Akanani ndi Aperizi. Ine ndilibe anthu ambiri, tsono iwoŵa akaitanizana kuti adzandithire nkhondo, ine ndi banja langa lonse, tonse pamodzi tidzaonongeka.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yakobo anati kwa Simeoni ndi Levi, Mwandisautsa ndi kundinukhitsa ine mwa anthu okhala m'dzikomu, mwa Akanani ndi mwa Aperizi; ndipo ine ndine wa anthu owerengeka, adzandisonkhanira ine ndi kundikantha: ndipo ndidzapasulidwa ine ndi a pa nyumba yanga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamenepo Yakobo anati kwa Simeoni ndi Levi, “Mwandiputira mavuto, ndi kundiyipitsira dzina pakati pa anthu a mʼdziko lino, Akanaani ndi Aperezi. Ife ndife owerengeka, ndipo atati aphatikizane kudzandithira nkhondo, ndiye kuti ine ndi banja langa tidzawonongeka.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yakobo anati kwa Simeoni ndi Levi, Mwaodisautsa ndi kundinunkhitsa ine mwa anthu okhala m'dzikomu, mwa Akanani ndi mwa Aperezi; ndipo ine ndine wa anthu owerengeka, adzandisonkhanira ine ndi kundikantha: ndipo ndidzapasulidwa ine ndi a pa nyumba yanga.