Genesis 34:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yakobe adaamva kuti Dina mwana wake adamgwiririra, koma popeza kuti ana ake aamuna anali ku busa kuŵeta ng'ombe, sadachitepo kanthu mpaka iwowo atabwera.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anamva Yakobo kuti anamuipitsa Dina, mwana wake wamkazi; ana ake amuna anali ndi zoweta zake kudambo: ndipo Yakobo anakhala chete mpaka anafika iwo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yakobo anamva kuti mwana wake Dina wagwiriridwa, koma sanachitepo kanthu msanga kudikira mpaka ana ake amuna omwe anali ku busa atabwerako.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anamva Yakobo kuti anamuipitsa Dina, mwana wace wamkazi; ana ace amuna anali ndi zoweta zace kudambo: ndipo Yakobo anakhala cete mpaka anafika iwo.