Genesis 34:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pa nthaŵi imeneyo ana ake a Yakobewo anali atangobwerako kubusa kuja. Anawo atamva zimenezo, adapsa mtima kwambiri. Adakwiya koopsa poona kuti Sekemu wachita chinthu choipa kwambiri ndi kuchita chipongwe Aisraele, pogwira Dina, mwana wa Yakobe, nkuchita naye zoipa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pakumva icho ana ake amuna a Yakobo anabwera pochokera kudambo: amunawo ndipo anapwetekwa mtima, nakwiya kwambiri, chifukwa iyeyo anachita chopusa choipira Israele pakugona ndi mwana wamkazi wa Yakobo; ndicho chosayenera kuchita.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa nthawi iyi nʼkuti ana a Yakobo atabwererako ku busa kuja. Iwo atangomva zimene zinachitika, anawawidwa mtima. Iwo anapsa mtima kwambiri kuti Sekemu nʼkuchita chonyansa choterechi mu dziko la Israeli, kumugwirira Dina, mwana wa Yakobo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pakumva ico ana ace amuna a Yakobo anabwera pocokera kudambo: amunawo ndipo anaphwetekwa mtima, nakwiya kwambiri, cifukwa iyeyo anacita copusa coipira Israyeli pakugona ndi mwana wamkazi wa Yakobo; ndico cosayenera kucita.