Genesis 35:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Mulungu adauza Yakobe kuti, “Nyamuka, pita ku Betele, ukakhale komweko. Ukamangeko guwa la Mulungu amene adakuwonekera pamene unkathaŵa mbale wako Esau.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Mulungu anati kwa Yakobo, Nyamuka nukwere kunka ku Betele nukhale kumeneko: numange kumeneko guwa la nsembe la Mulungu amene anaonekera kwa iwe pamene unathawa ku nkhope ya Esau mbale wako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono Mulungu anati kwa Yakobo, “Nyamuka uchoke kuno kupita ku Beteli. Kumeneko ukamange guwa lansembe la Mulungu amene anadza kwa iwe pamene umathawa Esau, mʼbale wako.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Mulungu anati kwa Yakobo, Nyamuka nukwere kunka ku Beteli nukhale kumeneko: numange kumeneko guwa la nsembe la Mulungu amene anaonekera kwa iwe pamene unathawa ku nkhope ya Esau mbale wako.