Genesis 35:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake Mulungu adamuuza kuti, “Ine ndine Mulungu, Mphambe. Ubale ana ambiri. Udzakhala ndi zidzukulu zambiri, ndipo zina mwa izo zidzakhala mafumu. Zidzukulu zako zidzachuluka kwambiri, kotero kuti zidzakhala mitundu yambiri ya anthu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Mulungu anati kwa iye, Ine ndine Mulungu Wamphamvuyonse: ubale, uchuluke; mwa iwe mudzatuluka mtundu ndi gulu la mitundu, ndipo mafumu adzatuluka m'chuuno mwako;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Mulungu anati kwa iye, “Ine ndine Mulungu Wamphamvuzonse; berekanani ndi kuchulukana. Mtundu wa anthu, inde, mitundu yambiri ya anthu idzatuluka mwa iwe, ndipo ena mwa zidzukulu zako adzakhala mafumu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Mulungu anati kwa iye, Ine ndine Mulungu Wamphamvuyonse: ubale, ucuruke; mwa iwe mudzaturuka mtundu ndi gulu la mitundu, ndipo mafumu adzaturuka m'cuuno mwako;