Genesis 35:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono onse adachoka ku Betele, koma asanafike ku Efurata, nthaŵi yoti Rakele aone mwana idamukwanira, ndipo kubereka kwake kudamuvuta kwambiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anachokera ku Betele: ndipo panatsala nthawi asanafike ku Efurata: ndipo Rakele anabala navutidwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka anachoka ku Beteli. Koma ali pafupi kufika ku Efurata nthawi yakuti Rakele aone mwana inakwana. Iye anavutika pobereka.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anacokera ku Beteli: ndipo panatsala nthawi asanafike ku Efrati: ndipo Rakele anabala nabvutidwa.