Genesis 35:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Rakele akumwalira kumene, akupuma mwaŵefuŵefu, kutsirizika, adamutcha mwanayo Benoni, koma bambo wake adamutcha Benjamini.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pakutsirizika iye, pakuti anamwalira, anamutcha dzina lake Benoni; koma atate wake anamutcha Benjamini.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono pamene Rakele ankapuma wefuwefu (popeza ankamwalira) iye anatcha mwana uja kuti Beni-Oni. Koma abambo ake anamutcha kuti Benjamini.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pakutsirizika iye, pakuti anamwalira, anamucha dzina lace Benoni; koma atate wace anamucha Benjamini.