Genesis 35:22 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene Yakobe ankakhala m'dziko limenelo, Rubeni adaachita zoipa ndi Biliha, mmodzi wa azikazi a bambo wake, Yakobeyo nkuzimva zimenezo. Yakobe anali ndi ana aamuna khumi ndi aŵiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo panali pamene Israele anakhala m'dzikomo, Rubeni anamuka nagona ndi Biliha, mkazi wamng'ono wa atate wake: ndipo Israele anamva. Ana amuna a Yakobo anali khumi ndi awiri:
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Israeli akanali mʼderali, Rubeni anapita nakagonana ndi Biliha, mdzakazi wa abambo ake. Yakobo uja anazimva zimenezi. Yakobo anali ndi ana aamuna khumi ndi awiri:
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo panali pamene Israyeli anakhala m'dzikomo, Rubeni anamuka nagona ndi Biliha, mkazi wamng'ono wa atate wace: ndipo Israyeli anamva. Ana amuna a Yakobo anali khumi ndi awiri: