Genesis 36:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
(Timna anali mzikazi wa Elifazi mwana wa Esau, ndipo mwa Timnayo Elifazi adaberekamo Amaleke.) Ameneŵa ndiwo ana a Ada mkazi wa Esau.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Timna anali mkazi wake wamng'ono wa Elifazi mwana wamwamuna wa Esau; ndipo anambalira Elifazi Amaleke: amenewa ndi ana amuna a Ada mkazi wake wa Esau.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Timna anali mzikazi wa Elifazi, mwana wa Esau. Iyeyo anaberekera Elifazi mwana dzina lake Amaleki. Amenewa ndiwo zidzukulu za Ada, mkazi wa Esau.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Timna anali mkazi wace wamng'ono wa Elifazi mwana wamwamuna wa Esau; ndipo anambalira Elifazi Amaleki: amenewa ndi ana amuna a Ada mkazi wace wa Esau.