Genesis 36:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mwa ana a Oholibama, mkazi wa Esau, panali mafumu aŵa: Yeusi, Yalamu ndi Kora. Ameneŵa ndiwo mafumu amene mkazi wa Esau, Oholibama mwana wa Ana, adabala.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Amenewa ndi ana amuna a Oholibama mkazi wake wa Esau; mfumu Yeusi, mfumu Yalamu, mfumu Kora, amenewa ndi mafumu obadwa kwa Oholibama mwana wamkazi wa Ana, mkazi wake wa Esau.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mwa ana a Oholibama, mkazi wa Esau munali mafumu awa: Yeusi, Yolamu, ndi Kora. Amenewa anali mafumu mwa ana a mkazi wa Esau, Oholibama, mwana wa Ana.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Amenewa ndi ana amuna a Oholibama mkazi wace wa Esau; mfumu Jeusi, mfumu Jalamu, mfumu Kora, amenewa ndi mafumu obadwa kwa Oholibama mwana wamkazi wa Ana, mkazi wace wa Esau.