Genesis 36:24 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ana a Zibiyoni ndi aŵa: Aya ndi Ana. (Ameneyu ndiye Ana amene adapeza akasupe otentha m'chipululu, pamene ankadyetsa abulu a Zibiyoni bambo wake.)
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ana a Zibiyoni ndi amenewa: Aiya ndi Ana; ameneyo ndiye Ana uja anapeza akasupe a madzi amoto m'chipululu, pakudyetsa abulu a Zibiyoni atate wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ana aamuna a Zibeoni anali awa: Ayiwa ndi Ana. Uyu ndi Ana amene anapeza akasupe a madzi amoto mʼchipululu pamene ankadyetsa abulu abambo wake Zibeoni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ana a Zibeoni ndi amenewa: Aia ndi Ana; ameneyo ndiye Ana uja anapeza akasupe a madzi amoto m'cipululu, pakudyetsa aburu a Zibeoni atate wace.