Genesis 36:35 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Atafa Husamu, Hadadi mwana wa Bedadi adaloŵa ufumu m'malo mwake. Iyeyu ndiye amene adagonjetsa Amidiyani m'dziko la Mowabu, ndipo dzina la mzinda wake linali Aviti.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Husamu anamwalira, ndipo Hadadi mwana wamwamuna wa Bedadi, amene anakantha Midiyani m'dambo la Mowabu, analamulira m'malo mwake: dzina la mudzi wake ndi Aviti.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Husamu atamwalira, Hadadi mwana wa Bedadi, amene anagonjetsa Amidiyani mʼdziko la Mowabu, analowa ufumu mʼmalo mwake. Mzinda wake unkatchedwa Aviti.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Husami anamwalira, ndipo Hadadi mwana wamwamuna wa Bedadi, amene anakantha Midyani m'dambo la Moabu, analamulira m'malo mwace: dzina la mudzi wace ndi Avita.