Genesis 36:39 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Baala-Hanani mwana wa Akibori atafa, Hadari ndiye adaloŵa ufumu m'malo mwake. Dzina la mzinda wake linali Pau, ndipo dzina la mkazi wake linali Mehetabele, mwana wa Matiredi mwana wa Mezahabu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Baala-Hanani mwana wamwamuna wa Akibori anamwalira, ndipo Hadari analamulira m'malo mwake; dzina la mudzi wake ndi Pau; ndipo dzina la mkazi wake ndi Mehetabele, mwana wamkazi wa Matiredi, mwana wamkazi wa Mezahabu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene Baala-Hanani mwana wa Akibori anamwalira, Hadari analowa ufumu mʼmalo mwake. Mzinda wake unkatchedwa Pau, ndipo dzina la mkazi wake linali Mehatabeli, mwana wamkazi wa Matiredi, mwana wamkazi wa Me-Zahabu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Baal-hanani mwana wamwamuna wa Akibori anamwalira, ndipo Hadari analamulira m'malo mwace; dzina la mudzi wace ndi Pau; ndipo dzina la mkazi wace ndi Mehetabeli, mwana wamkazi wa Matiredi, mwana wamkazi wa Me-zahabi.