Genesis 36:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Esau adatenga akazi ake, ana ake aamuna, ana ake aakazi ndi anthu onse a m'nyumba mwake, pamodzi ndi zoŵeta zake zonse, ndi katundu wake yense amene adampeza ku dziko la Kanani, ndipo adasiyana ndi mbale wake uja Yakobe, napita kukakhala ku dziko lina.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Esau anatenga akazi ake, ndi ana ake amuna, ndi ana ake akazi, ndi anthu onse a m'banja mwake, ndi ng'ombe zake, ndi zoweta zake, ndi zonse anali nazo anasonkhanitsa m'dziko la Kanani; ndipo ananka ku dziko losiyana patali ndi Yakobo mphwake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Esau anatenga akazi ake, ana ake aamuna ndi aakazi ndi ena onse a pa banja pake. Anatenganso ziweto zake ndi ziweto zake zonse pamodzi ndi katundu wake yense amene anamupata ku Kanaani, ndipo anachoka ku dziko la Kanaani kupatukana ndi mʼbale wake Yakobo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Esau anatenga akazi ace, ndi ana ace amuna, ndi ana ace akazi, ndi anthu onse a m'banja mwace, ndi ng'ombe zace, ndi zoweta zace, ndi zonse anali nazo anasonkhanitsa m'dziko la Kanani; ndipo ananka ku dziko losiyana patari ndi Yakobo mphwace.