Genesis 36:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chimene adachokera ndi chakuti dziko limene ankakhalako iye pamodzi ndi Yakobe, silinkaŵakwanira aŵiriwo. Anali ndi zoŵeta zochuluka zedi, mwakuti sikudatheke kuti iwo akhale pa malo amodzi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chuma chao chinali chambiri chotero kuti sanakhoze kukhala pamodzi; ndipo dziko lokhalamo iwo silinakhoza kuwakwanira chifukwa cha ng'ombe zao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo anatero chifukwa dziko limene ankakhalamo silikanakwanira awiriwo. Iwowa anali ndi ziweto zochuluka motero kuti sakanatha kukhala pamodzi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cuma cao cinali cambiri cotero kuti sanakhoza kukhala pamodzi; ndipo dziko lokhalamo iwo silinakhoza kuwakwanira cifukwa ca ng'ombe zao.