Genesis 37:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Abale ake aja adamuwonera kutali, iye asanayandikire nkomwe pamene panali iwopo. Adayamba kumpangira chiwembu natsimikiza zoti amuphe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo iwo anamuona iye ali patali, ndipo asanayandikire pafupi ndi iwo, anampangira iye chiwembu kuti amuphe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Abale ake aja anamuonera patali. Ndipo asanafike nʼkomwe kumene kunali iwo kuja, anayamba kale kumupangira chiwembu choti amuphe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo iwo anamuona iye ali patari, ndipo asanayandikire pafupi ndi iwo, anampangira iye ciwembu kuti amuphe.