Genesis 37:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mbiri ya banja la Yakobe ndi iyi: Pamene Yosefe anali mnyamata wa zaka 17, ankaŵeta nkhosa ndi mbuzi pamodzi ndi abale ake, ana a Biliha aja ndi a Zilipa, akazi aang'ono a bambo wake. Tsono Yosefeyo ankauza bambo wake zoipa zimene ankachita abale akewo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mibadwo ya Yakobo ndi iyi; Yosefe anali wa zaka khumi ndi zisanu ndi ziwiri analinkudyetsa zoweta pamodzi ndi abale ake; ndipo anali mnyamata pamodzi ndi ana a Biliha, ndi ana amuna a Zilipa, akazi a atate wake; ndipo Yosefe anamfotokozera atate wake mbiri yao yoipa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mbiri ya banja la Yakobo ndi iyi: Yosefe, mnyamata wa zaka 17 ankaweta nkhosa ndi abale ake, pamodzi ndi ana a Biliha ndi Zilipa, akazi a abambo ake. Tsono Yosefe ankabwera kudzawuza abambo ake zoyipa za abale ake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mibadwo ya Yakobo ndi iyi: Yosefe anali wa zaka khumi ndi zisanu ndi ziwiri analinkudyetsa zoweta pamodzi ndi abale ace; ndipo anali mnyamata pamodzi ndi ana a Biliha, ndi ana amuna a Zilipa, akazi a atate wace; ndipo Yosefe anamfotokozera atate wace mbiri yao yoipa.