Genesis 37:25 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene iwo ankadya, adaona gulu la Aismaele akuchokera ku Giliyadi. Ngamira zao zinali zitasenza nzonono ndi zonunkhira zimene ankapita nazo ku Ejipito.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo iwo anakhala pansi kuti adye chakudya; ndipo anatukula maso ao, nayang'ana, ndipo taonani, ulendo wa Aismaele anachokera ku Giliyadi ndi ngamira zao, zilinkunyamula zonunkhira ndi mafuta amankhwala ndi mure alinkumuka kutsikira nazo ku Ejipito.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Atakhala pansi kuti adye chakudya, anatukula maso naona gulu la Aismaeli akubwera kuchokera ku Giliyadi. Ngamira zawo zinanyamula zonunkhiritsa bwino zakudya zamitundumitundu, ndipo zimenezi ankapita nazo ku Igupto.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo iwo anakhala pansi kuti adye cakudya; ndipo anatukula maso ao, nayang'ana, ndipo taonani, ulendo wa Aismayeli anacokera ku Gileadi ndi ngamila zao, zilinkunyamula zonunkhira ndi mafuta amankhwala ndi libano alinkumuka kutsikira nazo ku Aigupto.