Genesis 37:26 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Yuda adafunsa abale ake kuti, “Kodi tipindulanji tikamupha mbale wathuyu ndi kubisa, osaulula kuti tamupha?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yuda anati kwa abale ake, Nanga tidzapindulanji tikamupha mbale wathu ndi kufotsera mwazi wake?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yuda anafunsa abale ake nati, “Kodi tidzapindula chiyani tikapha mʼbale wathuyu ndi kuphimbitsa magazi ake?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yuda anati kwa abale ace, Nanga tidzapindulanji tikamupha mbale wathu ndi kufotsera mwazi wace?