Genesis 37:27 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tiyeni timgulitse kwa Aismaeleŵa. Nanga iyeyu si mbale wathu, thupi limodzi ndiponso magazi amodzi?” Abale akewo adavomereza zimenezo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tiyeni timgulitse iye kwa Aismaele, tisasamulire iye manja; chifukwa ndiye mbale wathu, thupi lathu. Ndipo anamvera iye abale ake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Bwanji timugulitse kwa Aismaeliwa, koma ife tisamuchite kanthu kalikonse. Ameneyu ndi mʼbale wathu thupi limodzi ndi ife.” Abale ake anavomereza zimenezi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tiyeni timgulitse iye kwa Aismayeli, tisasamulire iye manja; cifukwa ndiye mbale wathu, thupi lathu. Ndipo anamvera iye abale ace.