Genesis 37:28 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Amidiyani ena amalonda adafika pomwepo. Abale akewo adamtulutsa Yosefeyo m'chitsime muja, namgulitsa kwa Aismaelewo pamtengo wokwana masekeli a siliva makumi aŵiri, ndipo iwowo adapita naye ku Ejipito.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anapita pamenepo Amidiyani a malonda: ndipo anamtulutsa namkweza Yosefe m'dzenjemo, namgulitsa kwa Aismaele ndi masekeli a siliva makumi awiri; ndipo ananka naye Yosefe ku Ejipito.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Amalonda ena a ku Midiyani ankadutsa pomwepo. Tsono abale ake a Yosefe anamutulutsa Yosefe uja mu chitsime chija ndipo anamugulitsa kwa Aismaeli aja pamtengo wa masekeli makumi awiri. Choncho anapita naye Yosefe ku Igupto.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ana pita pamenepo Amidyani a malonda: ndipo anamturutsa namkweza Yosefem'dzenjemo, namgulitsa kwa Aismayeli ndi ndalama zasiliva makumi awiri; ndipo ananka naye Yosefe ku Aigupto.