Genesis 37:35 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ana ake onse aamuna ndi aakazi, adabwera kuti amtonthoze koma iye adakana, adati, “Ndidzakhala ndikulira mwana wanga mpaka kumanda komwe kuli iyeko.” Choncho adapitirirabe kulira chifukwa cha Yosefe mwana wake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ana amuna ake onse ndi ana akazi onse anauka kuti amtonthoze: koma anakana kutonthozedwa; ndipo anati, Pakuti ndidzatsikira kumanda kwa mwana wanga, ndilinkulirabe. Atate wake ndipo anamlirira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngakhale kuti ana ake onse aamuna ndi aakazi anasonkhana kudzamutonthoza, iye anakana kutonthozedwa. Iye anati, “Ayi. Ndidzalira mpaka ndidzapite kwa mwana wanga ku manda.” Choncho Israeli anapitirirabe kulira mwana wake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ana amuna ace onse ndi ana akazi onse anauka kuti amtonthoze: koma anakana kutonthozedwa; ndipo anati, Pakuti ndidzatsikira kumanda kwa mwana wanga, ndirinkulirabe. Atate wace ndipo anamlirira.