Genesis 37:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Abale ake ataona kuti bambo wao ankakonda Yosefe kupambana iwowo, adayamba kudana naye Yosefeyo, ndipo sankalankhula naye mokondwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo abale ake anaona kuti atate wake anamkonda iye koposa abale ake onse: ndipo anamuda iye, ndipo sanathe kulankhula ndi iye mwamtendere.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene abale ake anaona kuti abambo awo ankakonda Yosefe kuposa aliyense wa iwo, anayamba kumuda Yosefe ndipo sankayankhula naye zamtendere.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo abale ace anaona kuti atate wace anamkonda iye koposa abale ace onse: ndipo anamuda iye, ndipo sanathe kulankhula ndi iye mwamtendere.