Genesis 37:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo abale akewo adamufunsa kuti, “Kodi ukuganiza kuti udzakhala mfumu yathu? Kodi ndiye kuti iweyo nkudzatilamula ife?” Motero adadana naye koposa kale chifukwa cha malotowo ndi mau akewo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Abale ake ndipo anati kwa iye, Kodi udzakhala mfumu yathu ndithu? Kapena udzatilamulira ife ndithu kodi? Ndipo anamuda iye koposa chifukwa cha maloto ake ndi mau ake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Abale ake aja anamufunsa nati, “Kodi ukuyesa kuti ungakhale mfumu yathu? Ungadzatilamuliredi iweyo?” Ndipo anamuda kuposa kale chifukwa cha maloto ake ndi zimene ankakonda kunena kwa abambo awo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Abale ace ndipo anati kwa iye, Kodi udzakhala mfumu yathu ndithu? kapena udzatilamulira ife ndithu kodi? ndipo anamuda Iye koposa cifukwa ca maloto ace ndi mau ace.