Genesis 38:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo Yuda adauza mpongozi wake uja Tamara kuti, “Bwererani kunyumba kwa bambo wanu, mukakhale wamasiye kumeneko mpaka mwana wanga Sela atakula.” Adanena zimenezi chifukwa ankaopa kuti Sela angafenso monga abale akewo. Motero Tamara adabwerera kunyumba kwa bambo wake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yuda anati kwa Tamara mpongozi wake, Khala wamasiye m'nyumba ya atate wako, kufikira akakula msinkhu Sela mwana wanga wamwamuna: chifukwa anati kuti, Angafe iyenso monga abale ake. Ndipo Tamara ananka nakhala m'nyumba ya atate wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka Yuda anati kwa mpongozi wake Tamara, “Bwererani ku nyumba ya abambo anu ndi kukhala kumeneko ngati wamasiye mpaka mwana wanga Sela atakula.” Ananena izi chifukwa ankaopa kuti Sela angafenso ngati abale ake aja. Choncho Tamara anapita kukakhala ku nyumba ya abambo ake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yuda anati kwa Tamara mpengozi wace, Khala wamasiye m'nyumba ya atate wako, kufikira akakula msinkhu Sela mwana wanga wamwamuna; cifukwa anati kuti, Angafe iyenso monga abale ace. Ndipo Tamara ananka nakhala m'nyumba ya atate wace.