Genesis 38:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Patapita nthaŵi, mkazi wa Yuda uja, mwana wa Suwa, adamwalira. Tsono Yuda atatha kulira malirowo, iyeyo pamodzi ndi bwenzi lake Hira Mwadulamu, adapita ku Timna kumene ankameta nkhosa zake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Atachuluka masiku mwana wamkazi wa Suwa, mkazi wake wa Yuda anafa; ndipo Yuda anatonthola mtima, nakwera kunka kwa akusenga nkhosa zake ku Timna, iye ndi bwenzi lake Hira, Mwadulamu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Patapita nthawi yayitali, Batishua, mkazi wa Yuda anamwalira. Yuda atatha kulira maliro a mkazi wake, anapita, iyeyu pamodzi ndi bwenzi lake Hira, Mwadulamu uja, ku Timna kumene ankameta nkhosa zawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Atacuruka masiku mwana wamkazi wa Sua, mkazi wace wa Yuda anafa; ndipo Yuda anatonthola mtima, nakwera kunka kwa akusenga nkhosa zace ku Timna, iye ndi bwenzi lace Hira, M-adulami.