Genesis 38:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Tamarayo adasintha zovala zake zaumasiye zija navala zina. Adadziphimba kumaso ndi nsalu, nakakhala pansi pa chipata cha ku Enaimu. Mudzi wa Enaimu unali pa mseu wopita ku Timna. Adaadziŵa kuti pa nthaŵiyo nkuti Sela atakula, komabe Tamara anali asanamloŵe chokolo Sela uja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo anavula zovala zake zamasiye, nadzifunda ndi chofunda chake, navala nakhala pa chipata cha Enaimu, chifukwa chili pa njira ya ku Timna; pakuti anaona kuti Sela anakula msinkhu, ndipo sanampatse iye kuti akhale mkazi wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
iye anavula zovala zake za umasiye, nadziphimba nkhope ndi nsalu kuti asadziwike, ndipo anakhala pansi pa chipata cha ku Enaimu popita ku Timna. Tamara anachita izi chifukwa anaona kuti ngakhale Selayo anali atakula tsopano, iye sanaperekedwe kuti amulowe chokolo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo anabvula zobvala zacezamasiye, nadzipfundandi copfunda cace, nabvala nakhala pa cipata ca Enaimu, cifukwa ciri pa njira ya ku Timna; pakuti anaona kuti Sela anakula msinkhu, ndipo sanampatsa iye kuti akhale mkazi wace.