Genesis 38:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yuda atamuwona, adaamuyesa mkazi wadama, chifukwa anali atadziphimba kumaso.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamene Yuda anamuona iye, anaganizira kuti ali mkazi wadama: chifukwa iye anabisa nkhope yake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yuda atamuona anangomuyesa mkazi wadama chabe, chifukwa anadziphimba nkhope.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamene Yuda anamuona iye, anaganizira kuti ali mkazi wadama: cifukwa iye anabisa nkhope yace.