Genesis 38:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adapita ku mbali ya mseu komwe kunali iyeyo namuuza kuti, “Kodi mungandilole kuti ndigone nanu?” Yuda sankadziŵa kuti ndi mpongozi wake. Mkaziyo adati, “Mudzandipatsa chiyani?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo iye anapatukira kwa mkazi panjira, nati, Tiyetu, ndilowane nawe; chifukwa sanamdziwe kuti ndiye mpongozi wake. Ndipo anati, Kodi udzandipatsa ine chiyani kuti ulowane ndi ine.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono anapita kwa mkaziyo pamphepete pa msewu paja nati, “Tabwera ndigone nawe.” Apa Yuda sankadziwa kuti mkazi uja anali mpongozi wake. Ndiye mkazi uja anamufunsa Yuda nati, “Mudzandipatsa chiyani kuti ndigone nanu?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo iye anapatukira kwa mkazi panjira, nati, Tiyetu, ndilowane nawe; cifukwa sanamdziwa kuti ndiye mpongozi wace. Ndipo anati, Kodi udzandipatsa ine ciani kuti ulowane ndi ine.