Genesis 38:20 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake Yuda adatuma bwenzi lake kukapereka mbuzi ija, kuti mkazi uja amubwezere zikole zija. Koma bwenzi lakeyo sadakampeze mkaziyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yuda anatumiza kamwana kambuzi ndi dzanja la bwenzi lake Mwadulamu, kuti alandire chikole pa dzanja la mkazi; koma sanampeze iye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono Yuda anatuma bwenzi lake Mwadulamu uja ndi kamwana kambuzi kaja kuti akapereke kwa mkazi wadama uja, ndi kuti akatero amubwezere chikole chake chija. Koma atafika sanamupezepo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yuda anatumiza kamwana ka mbuzi ndi dzanja la bwenzi lace Madulami, kuti alandire cikole pa dzanja la mkazi; koma sanampeza iye.