Genesis 38:21 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adafunsa anthu akomweko kuti, “Kodi mkazi wadama amene ankakhala pambali pa mseu wopita ku Enaimu uja ali kuti?” Anthuwo adayankha kuti, “Chikhalire sipadakhale mkazi wadama pa malo amenewo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anafunsa amuna a pamenepo kuti, Ali kuti wadama uja anali pambali pa njira pa Enaimu? Ndipo iwo anati, Panalibe wadama pano.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anawafunsa anthu a komweko, “Kodi mkazi wadama uja amene ankakhala pambali pa msewu wa ku Enaimu, ali kuti?” Iwo anayankha, “Sipanakhalepo mkazi wa dama aliyense pano.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anafunsa amuna a pamenepo kuti, Ali kuti wadama uja anali pambali pa njira pa Enaimu? ndipo iwo anati, Panalibe wadama pano.