Genesis 38:23 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yuda adati, “Zinthu zimenezo atenge zikhale zake, kuwopa kuti anthu angadzatiseke. Ngakhale sudampeze mkaziyo, komabe ine ndidaamtumizira ndithu mbuziyi.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yuda anati, Azilandire kuti tingachitidwe manyazi: taona, ndinatumiza mwana uyu wa mbuzi, ndipo sunampeza iye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamenepo Yuda anati, “Mulekeni atenge zinthuzo zikhale zake, kuopa kuti anthu angatiseke. Ine sindinalakwe, ndinamutumizira kamwana kambuzika, koma simunamupeze.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yuda anati, Azilandire kuti tingacitidwe manyazi: taona, ndinatumiza mwana uyu wa mbuzi, ndipo sunampeza iye.