Genesis 38:25 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Akutengedwa kumene, Tamarayo adatumiza mau kwa Yuda mpongozi wake kuti, “Ine ndili ndi pathupi pa mwiniwake zinthu izi. Taziyang'anani, muwone mwina inu nkumudziŵa mwiniwakeyo kuti ndani: mpheteyi ndi chingwechi ndiponso ndodo yoyenderayi.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamene anamtulutsa iye, mkazi anatumiza kwa mpongozi wake kuti, Ndi mwamuna mwini izi ndatenga pakati; ndipo mkazi anati, Tayang'anatu, za yani zimenezi, mphete, ndi chingwe, ndi ndodo?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Akumutulutsa, iye anatuma mawu kwa apongozi ake. Anati, “Ndili ndi pathupi pa munthu amene ndi mwini wake wa zinthu izi. Taziyangʼanitsitsani, kodi mwini wa khoza, chingwe ndi ndodo yoyenderayi ndi yani?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamene anamturutsa Iye, mkazi anatumiza kwa mpongozi wace kuti, Ndi mwamuna mwini izi ndatenga pakati; ndipo mkazi anati, Tayang'anatu, za yani zimenezi, mphete, ndi cingwe, ndi ndodo?