Genesis 38:26 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yuda atazizindikira zinthuzo adati, “Akunenetsadi. Ndine amene ndidalakwa. Bwenzi nditampereka kwa mwana wanga Sela kuti amkwatire.” Choncho Yuda sadagone nayenso mkaziyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yuda anavomereza nati, Akhale wolungama wopambana ine, chifukwa ine sindinampatsa iye Sela mwana wanga wamwamuna. Ndipo iye sanamdziwenso mkaziyo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yuda anazizindikira zinthuzo ndipo anati, “Uyu ndi wolungama kuposa ine, chifukwa sindinamupereke kwa mwana wanga Sela.” Ndipo Yuda sanagone nayenso.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yuda anabvomereza nati, Akhale wolungama wopambana ine, cifukwa ine sindinampatsa iye Sela mwana wanga wamwamuna. Ndipo iye sanamdziwanso mkaziyo.